Chichewa pronunciation guide.
\a\ as a in father
\e\ as e in bed
\i\ as i in hit
\o\ as o in go
\u\ as u in put
--- Compiled by Harry Gombachika
* hello --- moni
* how are you ? --- muli bwanji ?
* I am fine --- ndiri bwino
* Thank you --- zikomo
* I am happy --- ndakondwa/ndili wokondwa/ndasangalala/ndili wosangalala
* I am sick/ill --- ndikudwala
* I have arrived --- ndafika
* I have departed - ndanyamuka
* I am tired - ndatopa
* I love you --- ndimakukonda/ndimakukondani
* I love you too --- ndimakukondanso/ndimakukondaninso
* God --- Mulungu/Chauta/Namalenga
* person --- munthu
* father --- bambo
* mother --- mayi
* child --- mwana
* boy --- mnyamata
* girl --- mtsikana
* garment --- chobvala (shirt, dress etc)
* shorts --- kabudula
* chilundu --- a piece of cloth wrapped round the waist covering from waist down.
* shoe(s) --- nsapato
* house --- nyumba
* aeroplane - ndege
* village --- mudzi
* country --- dziko
* way/ path --- njira
* road --- nseu
* bicycle --- njinga
* car --- galimoto
* plane --- ndenge
* eating - kudya
* food --- chakudya
* water --- madzi
* beer --- mowa
* meat --- nyama
* rice --- mpunga
* corn/maize --- chimanga
* fish --- nsomba
* salt --- mchere
* pepper --- tsabola
* tobacco --- fodya
* smoking - kusuta
* money --- ndalama
* ndalama zingati ? --- how much ? ( asking for a price of a commodity )
* lion --- mkango
* elephant --- njobvu
* zebra --- mbidzi
* buffalo --- njati
* crocodile --- ng'ona
* hippo --- mvuwu/bokho
* hare kalulu
* dog --- galu
* cat --- mphaka/chona/chome
* bird --- mbalame
* chicken --- nkhuku
* snake --- njoka
* frog --- chule
* toad --- finye
* tree --- mtengo
* chair --- mpando
* fence --- mpanda
* hoe handle --- mpini
* sarvior --- mpulumutsi
* knife --- mpeni
* cave --- phanga
* wing --- phiko
* germinate --- phuka
* parcel --- phukusi
* cook (verb) --- phika
* shoulder --- phewa
* run away --- thawa
* buttock --- thako
* a tale --- nthano
* solid rock --- thanthwe
* bed --- kama
* to milk --- kukama
* hoe --- khasu
* ear --- khutu
* pig --- nkhumba
* fire wood --- nkhuni
* to eat --- kudya
* to buy --- kugula
* to want --- kufuna
* to walk --- kuyenda
* to go --- kupita
* to sleep --- kugona
* to write --- kulemba
* to think --- kuganiza
* to steal --- kuba
* to drink --- kumwa
* to sing --- kuyimba
* to dance --- kuvina
* to jump --- kulumpha/kudumpha
* to walk --- kuyenda
* to laugh --- kuseka
* to read--- kuwerenga
* to runkuthamanga
* to lie --- kunama
* to put --- kuika
* to doubt --- kukayika
* to go --- kupita
* to come --- kubwera
* to send --- kutumiza
* to receive --- kulandira
* to hide --- kubisa
* to complain --- kudandaula
Miyambi --- Proverbs
* Chikomekome cha mkuyu, mkati muli nyerere==Appearances often deceives
* Akulu ndi mdambo mozimira moto
* Mutu ukakula sulewa nkhonya
* Lero lomwe lidadetsa nthengu
* Muluzu wa galu ndi umodzi
* Guluwe inalira msampha utaning'a
* Mbuto ya kalulu inakula mtadzaonani
* Ulenji umasimba wako
* Kulasa mtengo mchamuna chomwe
* Phukusi la moyo sasungilana
* Fodya wako ndi uyo ali pamphuno, wam'manja ngwa mphepo
* Ukayendera mzengo usamati asakhwi a fumbula
* Khwangwala wa mantha, anafa ndi ukalamba
* Kwaweni kukudyetsa nthanga, dzungu ukuliwona
* Guwo yobwera samagwira banja
* Chimanga chimalola opanda manu
* Mutu umodzi susenza denga
* Chala chimodzi sichiswa msabwe
* Ulidele nkulinga utayenda naye
* Watchera kumwezi, nkhanga zawona
* Wokaona nyanja anakaona mvuwu
* Awonenji anapha mvuvu ndi phuma
* Wopenga anaona nkhondo
* Chinasala chinalaka fisi
* Phongo ya chiwala siyichepa
* Pagona tode padzinukha
* Timba sachepa ndi mazira ake
* Timba anathyoka mwendo mphando litatha kale
* Papsa tong'ola sudziwa mtima wa moto
* Moto umapita kuli ntchire
* thumba la tambe amasula ndi tambe yemwe
* Mumandiyitana pakalowa njoka, pakalowa mbewa mumakumba nokha
* Mulendo ndi amene akhala ndi kampeni ka kutwa
* Chikondi cha nkhwangwa, chokoma pokwera
* Chiri kwa nzako, nkumati chigwire nyanga
* Ichi chakoma, ichi chakoma, pusi anagwa chagada
* Akule bvumbe wotatha pa tsekera
* Kumpha mbalame ziwiri ndi mwala umodzi
* Khoswe akakhala pa mkhate sapheka
* mbalame ikatera pauta silasika
* Chibale nchipsera sichitha
* Anasi ndi nkhondo
* Kalulu anatuma njobvu
* nyimbo imodzi sachezera gule
* Umanena chatsitsa dzaye, kuti njobvu ithyoke mnyanga
* Pang'ono pang'ono, tsokonombwe anatha mtunda mkudumpha
* Fisi anakana msatsi
* Chidakwa chinakana kulipira ngongole ya thobwa
* Dazi lilibe mankhwala
* Madzi akatayika sawoleka
* Kwanu ndi kwanu, mthengo munalaka njoka
* Tsamba likagwa, manyazi agwira mtengo
* Tsabola wakale sawawa
* Kuno ndi kunja, kuyanja lichero
* Nkhuyu zodya ana, zipota akulu
* Mako ndi mako, usamuone kuchepa mwendo
* Tsoka sasimba
* Tsoka likalimba, umakuwotcha ndi mkute
* Mwana wa nzako ndiwako yemwe, ukachenjera manja, udya naye
* Mamuna nzako mpachulu, nkulinga utakwerapo
* Tsiku limodzi siliwoza mbewa
* Nkhoswe wa pa denga anaulula wa padzala
* Ukakwera pansana wa njobvu, usamati kulibe mame
* Buluzi wa mnyenyo anapanidwa ndi chitseko
* Lunga lunga pobwadwa, chilema chichita kudza
* Chuma ndi mchira wa khoswe, suchedwa kupululuka
* Pati bi, pali minga
Mikuliwiko---Figurative Expressions
* Kanga ndiwamba
* Mbiya ngambe--chidakwa==drunkard
* Chiphadzuwa--ngenge-- beautiful girl/lady
* Konsekonse mpeni wansengwa--mthira kuwiri== showing double standards
* Bowa bwanga-- kukayika== to hastate
* mtentha ndebvu === tea
* Kukhomera ku Dowa-- kusabereka--
This is all at the moment. I hope these words/phrases will be helpful.
Zikomo kwambiri ---- thank you very much